Kodi kutchova juga ndi tchimo?

Kodi Kutchova Juga Ndi Tchimo?


Yankho la m'Baibulo

Ngakhale kuti Baibulo silifotokoza mwatsatanetsatane zokhudza juga, mfundo za m'Baibulo zingatithandize kuzindikira kuti Mulungu amaona kuti khalidweli ndi tchimo. -Aefeso 5:17.

Anthu amatchova juga chifukwa cha dyera ndipo Mulungu amadana ndi khalidwe limeneli. (1 Akorinto 6:9, 10; Aefeso 5:3, 5) Kuti munthu wotchova juga awine, pamafunika kuti anzake aluze, koma Baibulo limaletsa kusirira zinthu za anthu ena mwansanje. -Ekisodo 20:17; Aroma 7:7; 13:9, 10.

Kutchova juga, ngakhale pang'ono pokha, kungachititse munthu kuti ayambe kukonda kwambiri ndalama. -1 Timoteyo 6:9, 10.

Nthawi zambiri anthu otchova juga amadalira matsenga kapena mwayi. Komabe, Mulungu amaona kuti kukhulupirira zimenezi ndi kulambira mafano, komwe sikugwirizana ndi kulambira kumene iye amavomereza. -Yesaya 65:11.

M'malo molimbikitsa khalidwe lomapeza zinthu zomwe sitinazigwirire ntchito, Baibulo limatilimbikitsa kugwira ntchito mwakhama. (Mlaliki 2:24; Aefeso 4:28) Anthu omwe amatsatira malangizowa "amadya chakudya chimene achigwirira ntchito." -2 Atesalonika 3:10, 12.

Kutchova juga kumalimbikitsa khalidwe la mpikisano, lomwe limaletsedwa m'Baibulo. -Agalatiya 5:26.